UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Fufuzani Kuti Mudziŵe Maganizo a Mulungu
Timafuna kukondweletsa Yehova m’zocita zathu zonse. (Miy. 27:11) Koma kuti ticite zimenezi, tiyenela kupanga zisankho zogwilizana na maganizo ake, ngakhale kuti palibe lamulo lacindunji lotitsogolela pankhaniyo. Kodi n’ciyani cingatithandize kucita zimenezi?
Muziŵelenga Baibo nthawi zonse. Nthawi zonse tikamaŵelenga Baibo, zimakhala ngati tikuceza na Yehova. Tingadziŵe maganizo a Yehova mwa kuona mmene anacitila zinthu na anthu ake komanso kusinkhasinkha zitsanzo za anthu amene anacita zabwino kapena zoipa pamaso pake. Tikafuna kupanga cisankho, mzimu woyela ungatithandize kukumbukila mfundo zofunika zimene tinaphunzila m’Mawu a Mulungu.—Yoh. 14:26.
Fufuzani. Mukafuna kupanga cisankho, dzifunseni kuti, ‘Kodi ni mavesi ati kapena zocitika ziti zochulidwa m’Baibo zimene zinganithandize kumvetsa mmene Yehova amaonela nkhaniyi?’ Pemphani thandizo kwa Yehova, ndipo seŵenzetsani zida zofufuzila zimene zilipo m’cinenelo canu kuti zikuthandizeni kupeza mfundo za m’Baibo. Zidazo zingakuthandizeninso kuona mmene mungagwilitsile nchito mfundozo popanga cisankho canu.—Sal. 25:4.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI TIFUNIKA “KUTHAMANGA MOPILILA”—IDYANI ZAKUDYA ZOPATSA THANZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
Ni mavuto otani amene mlongo wacitsikana wa m’vidiyoyi anakumana nawo?
-
Kodi mungaseŵenzetse bwanji zida zofufuzila kuti zikuthandizeni kulimbana na mavuto monga amene mlongoyu anakumana nawo?
-
Kodi timapindula bwanji ngati tipatula nthawi yofufuza na kucita phunzilo la munthu mwini kuti tipeze mfundo zotithandiza kupanga zisankho zabwino?—Aheb. 5:13, 14