Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Mawu a Mulungu

Limbitsani Cikhulupililo Canu pa Mawu a Mulungu

Mawu a Mulungu angasinthe umoyo wathu. (Aheb. 4:12) Komabe, kuti tipindule na malangizo ake komanso uphungu wake, tiyenela kukhutila kuti Baibo ni ‘mawudi a Mulungu.’ (1Tim. 2:13) Kodi tingacite ciyani kuti tiziikhulupilila kwambili Baibo?

Muziiŵelenga tsiku lililonse. Pamene muŵelenga, yesetsani kupeza umboni wakuti Yehova ndiye Mlembi wake. Mwacitsanzo, ganizilani malangizo anzelu opezeka m’buku la Miyambo, na kuona mmene amatithandizila pa umoyo wathu masiku ano.—Miy. 13:20; 14:30.

Muzisankha nkhani na kuiphunzila mozama. Dziŵani bwino umboni woonetsa kuti Baibo ni youzilidwadi. Mu Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, onani pa mutu wakuti “Baibo,” kenako pa “Inauzilidwa na Mulungu.” Mungalimbitsenso cikhulupililo canu cakuti uthenga wa m’Baibo sunasinthe mwa kuŵelenga nkhani yakuti, “Baibulo Lakumana ndi Zambili” mu Galamukani ya November 2007.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI CIFUKWA CAKE TIMAKHULUPILILA . . . MAWU A MULUNGU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:

  • Kodi cipupa ca kacisi cimene cinapezeka ku Karnak m’dziko la Egypt, cimatsimikizila bwanji kuti Mawu a Mulungu amakamba zoona?

  • Kodi tidziŵa bwanji kuti uthenga wa m’Baibo sunasinthe?

  • Baibo yapulumuka zambili. Kodi izi zimakuthandizani bwanji kutsimikizila kuti Baibo ni mawudi a Mulungu?—Ŵelengani Yesaya 40:8