January 2-8
2 MAFUMU 22-23
Nyimbo 28 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“N’cifukwa Ciyani Tiyenela Kukhala Odzicepetsa?”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
2 Maf. 23:24, 25—Kodi citsanzo ca Yosiya cingawalimbikitse bwanji anthu amene anakulila m’banja limene makolo sanali citsanzo cabwino? (w01 4/15 26 ¶3-4)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulila iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 2 Maf. 23:16-25 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Pemphelo—Sal. 65:2. Nthawi zonse vidiyo ikaima, inunso iimitseni na kufunsa omvela mafunso amene aonekela.
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. (th phunzilo 1)
Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. M’gaŵileni bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! na kuyambitsa phunzilo la Baibo m’phunzilo 01. (th phunzilo 16)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Ndinu Wodzicepetsa Kapena Wodzikuza? (Yak. 4:6): (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Kenako, funsani omvela mafunso awa: Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kudzicepetsa na kudzikuza? Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo ca Mose? N’cifukwa ciyani tiyenela kuyesetsa kukhalabe odzicepetsa?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 33
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 23 na Pemphelo