UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso
Masiku otsiliza ano, timakumana na mayeso ambili. Nthawi zina, tingaone monga kuti mayeso athu ni aakulu kwambili moti sitingakwanitse kuwapilila. Komabe, ngati tikhalabe pa ubale wolimba na Yehova, iye adzatithandiza kupilila mayeso ngakhale ovuta kwambili. (Yes. 43:2, 4) Kodi tingalimbitse bwanji ubale wathu na Yehova pamene tikumana na mayeso?
Pemphelo. Ngati tamukhuthulila za mumtima mwathu Yehova, adzatipatsa mtendele komanso mphamvu kuti tithe kupilila.—Afil. 4:6, 7; 1 Tim. 5:17.
Misonkhano. Kuposa kale lonse, masiku ano timafunikila kwambili cakudya cauzimu komanso mayanjano amene Yehova amapeleka pa misonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Tikamakonzekela misonkhano ya mpingo, kupezekako, na kutengako mbali, timapindula kwathunthu na thandizo la mzimu woyela wa Yehova.—Chiv. 2:29.
Ulaliki. Tikamacita zonse zotheka kuti tikhalebe okangalika mu ulaliki, cidzakhala cosavuta kuikabe maganizo athu pa zinthu zolimbikitsa. Kuwonjezela apo, tidzalimbitsa ubwenzi wathu na Yehova komanso anchito anzathu.—1 Akor. 3:5-10.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA ADZAKULANDILANI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
N’ciyani cinathandiza Malu kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova pamene anali kukumana na mayeso?
-
Mofanana na Malu, kodi mawu a pa Salimo 34:18 angatilimbikitse bwanji pamene tikukumana na mayeso?
-
Kodi zimene zinacitikila Malu zionetsa bwanji kuti Yehova amapeleka “mphamvu yoposa yacibadwa” tikakumana na mayeso?—2 Akor. 4:7