CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Khalanibe Maso
Kwa zaka zambili, Yehova anali kucenjeza Ayuda kuti adzawakana ngati apitiliza kucita zoipa (2 Maf. 24:2, 3; w01 2/15 12 ¶2)
Iye anagwilitsa nchito Ababulo powononga Yerusalemu mu 607 B.C.E. (2 Maf. 25:8-10; w07 3/15 11 ¶10)
Yehova anapulumutsa anthu amene analabadila macenjezo ake (2 Maf. 25:11)
Kwa zaka zambili, iye wakhala akucenjeza anthu padzikoli kuti adzawononga “anthu osaopa Mulungu.”—2 Pet. 3:7.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi nimaseŵenzetsa mpata uliwonse umene napeza kuthandiza anthu kulabadila cenjezo la Mulungu?’—2 Tim. 4:2.