Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

February 19-25

MASALIMO 8-10

February 19-25

Nyimbo 2 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Ndidzakutamandani Inu Yehova”!

(Mph. 10)

Yehova amaticitila zabwino koposa (Sal. 8:​3-6; w21.08 3 ¶6)

Timasangalala kuuzako ena nchito za Yehova zodabwitsa (Sal. 9:1; w20.05 23 ¶10)

Timamutamanda mwa kumuimbila mocokela pamtima (Sal. 9:2; w22.04 7 ¶13)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova ningamutamande m’njila zinanso ziti?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 8:3—Kodi wamasalimo anatanthauzanji pochula zala za Mulungu? (it-1 832)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 10:​1-18 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) NYUMBA NA NYUMBA. Mwininyumba wakuuzani kuti sakhulupilila kuti kuli Mulungu. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pa makambilano apita, munthuyo anakuuzani kuti sakhulupilila kuti kuli Mulungu, koma anati ni wololela kukambilana umboni woonetsa kuti Mlengi aliko. (th phunzilo 7)

6. Nkhani

(Mph. 5) w21.06 6-7 ¶15-18—Mutu: Thandizani maphunzilo anu a Baibo kutamanda Yehova. (th phunzilo 10)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 10

7. Mmene Mungacitile Ulaliki Wamwayi Mwacibadwa

(Mph. 10) Kukambilana.

Njila imodzi imene tingatamandile Yehova mowonjezeleka ni kulalikila anthu omwe timakumana nawo tsiku na tsiku. (Sal. 35:28) Poyamba tingacite mantha kulalikila mwamwayi. Komabe tikadziŵa moyambitsila makambilano mwacibadwa, tingakhale aluso ndipo tingamakondwele pocita zimenezi!

Tambitsani VIDIYO yakuti Muzikhala Wokonzeka Kuuzako Ena “Uthenga Wabwino wa Mtendele”—Muziyambitsa Ndinu Makambilano. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi mwaphunzilanji mu vidiyo iyi cokuthandizani kunola luso lanu pocita ulaliki wamwayi?

Nazi njila zina zomwe zingakuthandizeni kuyambitsa makambilano:

  •   Nthawi zonse mukacoka panyumba muzifunafuna mipata yoyambitsa makambilano. Ipempheleleni nkhaniyo, ndipo pemphani Yehova kuti akutsogoleleni kupeza anthu amene angamvetsele

  •   Khalani aubwenzi na kuŵaonetsa cidwi anthu amene mumakumana nawo. Yesani kumudziŵa munthuyo kuti muone mfundo ya m’Baibo imene angacite nayo cidwi

  •   Ngati n’zotheka yesani kupeza mpata wotenga fon’namba yake

  •   Musakhumudwe ngati makambilano atha musanamulalikile munthuyo

  •   Muziganizila munthuyo pambuyo pa makambilano anu. Pitilizani kumuonetsa cidwi mwa kumutumizila linki ya vesi ya m’Baibo kapena ya nkhani yopezeka pa jw.org

Yesani izi: Ngati wina wakufunsani kuti, ‘Kodi wikendi inali bwanji?,’ muuzen’koni zimene munaphunzila pa msonkhano kapena za nchito yanu yophunzitsa Baibo.

8. Zofunika za Mpingo

(Mph. 5)

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 65 na Pemphelo