February 5-11
MASALIMO 1-4
Nyimbo 150 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Khalani ku Mbali ya Ufumu wa Mulungu
(Mph. 10)
[Tambitsani VIDIYO yakuti Mfundo Zokhudza Buku la Masalimo.]
Maboma a anthu adzipanga okha kukhala adani a Ufumu wa Mulungu (Sal. 2:2; w21.09 15 ¶8)
Yehova akupatsa anthu onse mpata wakuti asankhe kukhala ku mbali ya Ufumu wake (Sal. 2:10-12)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndine wotsimikiza kusakhalila mbali pa ndale za dziko, ngakhale kuti zimenezi zinganibweletsele mavuto?’—w16.04 29 ¶11.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 1:4—Kodi anthu oipa ali ngati “mankhusu amene amauluzika ndi mphepo” m’lingalilo lotani? (it-1 425)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 3:1–4:8 (th phunzilo 12)
4. Kukamba Mwacibadwa—Mmene Filipo anacitila zimenezi
(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO yakuti kenako kambilanani lmd phunzilo 2 mfundo 1-2.
5. Kukamba Mwacibadwa—Tengelani Citsanzo ca Filipo
(Mph. 8) Makambilano ozikika pa lmd phunzilo 2 mfundo 3-5 komanso mbali yakuti “Onaninso Malemba Awa.”
Nyimbo 32
6. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 15)
7. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu. 5 ¶9-15, bokosi pa tsa. 41