January 15-21
YOBU 36-37
Nyimbo 147 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Cifukwa Cake Muyenela Kukhulupilila Lonjezo la Mulungu la Moyo Wosatha
(Mph. 10)
Yehova iye mwiniyo ni wamuyaya (Yobu 36:26; w15 10/1 13 ¶1-2)
Yehova ali na nzelu komanso mphamvu zocilikiza moyo (Yobu 36:27, 28; w20.05 22 ¶6)
Yehova amatiphunzitsa mmene tingapezele moyo wosatha (Yobu 36:4, 22; Yoh. 17:3)
Tikakhulupilila zolimba kuti Mulungu adzatipatsa moyo wosatha, sitidzasunthika pokumana na mavuto mu umoyo wathu.—Aheb. 6:19; w22.10 28 ¶16.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Yobu 37:20—Kodi mauthenga na nkhani zinali kufalitsidwa motani m’malo ochulidwa m’Baibo? (it-1 492)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4.) Yobu 36:1-21 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 3 mfundo 3)
5. Kubwelelako
(Mph. 4) NYUMBA NA NYUMBA. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila
(Mph. 5.) Nkhani. ijwfq 57 ¶5-15—Mutu: N’cifukwa ciyani Mboni za Yehova zinazunzidwa pa Cipululutso ca Nazi? (th phunzilo 18)
Nyimbo 49
7. Konzekelani Pali Pano Musanafunikile Cithandizo ca Mankhwala kapena Opaleshoni
(Mph. 15) Kukambilana. Ikambidwe na mkulu.
Gulu la Yehova latipatsa zida zotithandiza kumvela lamulo la Yehova pa nkhani ya magazi. (Mac. 15:28, 29) Kodi mumazigwilitsa nchito bwino?
Khadi Lopatsa Munthu Mphamvu Yosasinthika Yondisankhira Thandizo la Mankhwala (DPA) na Khadi ya Mwana (ic): Makhadi amenewa amafotokoza cisankho cimene munthu wapanga pa nkhani ya magazi. Ofalitsa obatizika angatenge khadi lawo la DPA komanso kutengela ana awo Makhadi a Ana kwa mtumiki wa mabuku. Makhadi amenewa tiyenela kuwanyamula kulikonse kumene tingapite. Ngati mukufuna kusaina khadi yanu kapena kuisintha, citani zimenezo mwamsanga.
Mfundo Zokhudza Azimayi Apathupi (S-401) komanso Malangizo kwa Odwala Ofunikila Opaleshoni Kapena Cithandizo ca Kemofelapi (S-407): Mafomuwa adzakuthandizani kupanga cisankho cabwino akafuna kukupatsani cithandizo ca mankhwala cimene cingafune magazi. Ngati muli na pathupi, mukuyembekezela kucitidwa opaleshoni, kapena kulandila cithandizo ca matenda a khansa, pemphani akulu kuti akupatseni fomu yoyenelela.
Komiti Yokambilana ni Acipatala (HLC): Amene amatumikila mu HLC ni akulu odziŵa bwino mofotokozela nkhani za magazi kwa madokotola komanso kwa ofalitsa. Angakambilane na madokotala za mankhwala kapena njila zothandizila odwala m’malo moika magazi. Pakakhala pofunika, angakuthandizeni kupeza dokotala yemwe angalemekeze cisankho canu. Iwo ni okonzeka kukuthandizani tsiku lililonse, komanso nthawi iliyonse. Mwamsanga dziŵitsani a HLC ngati mwadziŵa kuti adzakucitani adimiti, kukucitani opaleshoni, kapena cithandizo cina ca mankhwala—monga cithandizo pa matenda a khansa—ngakhale muona kuti sadzafunika kukuikani magazi. Nawonso azimayi apathupi ayenela kucita zimenezi. Mukafunikila thandizo, pemphani akulu kuti akupatseni nambala ya abale a mu HLC.
Tambitsani VIDIYO yakuti Makomiti Okambilana ni Acipatala—Kodi Amathandiza Bwanji? Kenako funsani omvela kuti:
Kodi a HLC angakuthandizeni bwanji mukafunikila cithandizo ca mankhwala kapena kucitidwa opaleshoni?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 4 ¶9-12, bokosi pa tsa. 34