Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

January 22-28

YOBU 38-39

January 22-28

Nyimbo 11 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Kodi Mumapatula Nthawi Kuyang’ana Zacilengedwe?

(Mph. 10)

Atalenga dziko lapansi, Yehova anapatula nthawi yoyang’ana zinthu zimene analenga (Gen. 1:​10, 12; Yobu 38:​5, 6; w21.08 9 ¶7)

Angelo nawonso anapatula nthawi yoyang’ana cilengedwe ca Yehova (Yobu 38:7; w20.08 14 ¶2)

Timalimbikitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova tikamapatula nthawi yoyang’ana zacilengedwe na kuziyamikila (Yobu 38:​32-35; w23.03 17 ¶8)

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 38:​8-10—Kodi mavesiwa aonetsa bwanji kuti Yehova ndiye woyenela kupeleka malamulo? (it-2 222)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 39:​1-22 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Thetsani makambilanowo mwaulemu mukaona kuti munthuyo safuna kukambilana. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 5) NYUMBA NA NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo anakuuzani kuti posacedwa anataikilidwa wokondedwa wake mu imfa. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd zakumapeto A mfundo 1—Mutu: Zocitika pa Dziko na Makhalidwe a Anthu Zionetsa Kuti Posacedwa Zinthu Zidzasintha. (th phunzilo 16)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 111

7. Kuyang’ana Zacilengedwe Kumatithandiza Kukhala na Maganizo Oyenela

(Mph. 15) Kukambilana.

Pamene Yobu anali kuvutitsidwa na Satana komanso anzake atatu, iye anali kuganizila kwambili mavuto ake na kunenezedwa kwake kopanda cilungamo.

Ŵelengani Yobu 37:14. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi Yobu anafunika kucita ciyani kuti akhalenso wolimba mwauzimu?

Tikalefulidwa na mayeso amene tingakumane nawo, kuyang’ana zacilengedwe kungatithandize kukumbukila ukulu wa Yehova, kulimbikitsa cikhumbo cathu cokhalabe wokhulipilika kwa iye, komanso kukulitsa cidalilo cathu cakuti iye ali na mphamvu zokwanitsa kutithandiza.—Mat. 6:26.

Tambitsani VIDIYO yakuti Zimene Tiphunzila pa Nkhani Yokhala Wokhulupilika m’Buku la Yobu—Pa Nyama Zimene Mulungu Analenga. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi vidiyo iyi yalimbikitsa bwanji cikhulupililo canu mwa Yehova?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 4 ¶13-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 54 na Pemphelo