Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

January 29–February 4

YOBU 40-42

January 29–February 4

Nyimbo 124 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Zimene Tiphunzilapo pa Zinacitikila Yobu

(Mph. 10)

Tizikumbukila kuti kapenyedwe kathu n’kopeleŵela polinganiza na Yehova (Yobu 42:​1-3; w10 10/15 3-4 ¶4-6)

Muzilandila uphungu wocokela kwa Yehova na gulu lake (Yobu 42:​5, 6; w17.06 25 ¶12)

Yehova amadalitsa anthu amene amakhulupilikabe pokumana na mayeso (Yobu 42:​10-12; Yak. 5:11; w22.06 25 ¶17-18)

Yehova anamufupa Yobu pokhala wokhulupilika

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 42:7—Pamene anzake atatu anali kumuneneza Yobu, kodi anali kuneneza ndani kwenikweni? (it-2 808)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 42:​1-17 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) NYUMBA NA NYUMBA. Munthuyo si wa cipembedzo cacikhristu. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)

5. Kupanga Ophunzila

6. Nkhani

(Mph. 4) lmd zakumapeto A mfundo 2—Mutu: Dziko Lapansi Silidzawonongedwa Konse. (th phunzilo 13)

UMUYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 108

7. Thandizani Ena Kudziŵa Kuti Yehova Amaŵakonda

(Mph. 15) Kukambilana.

Timakondwela kulambila Mulungu amene ndiye cikondi. (1 Yoh. 4:​8, 16) Cikondi ca Yehova cimatipangitsa kumuyandikila na kukhalabe naye pa ubwenzi. Pokhala nkhosa zake, tonsefe timadziŵa kuti Yehova amatikonda.

Mmene timacitila zinthu na acibale athu, alambili anzathu, komanso anthu ena zimaonetsa kuti timatengela cikondi ca Yehova kapena ayi. (Yobu 6:14; 1 Yoh. 4:11) Tikamaonetsa ena cikondi, timawathandiza kumudziŵa Yehova na kumuyandikila. Koma ngati sitiwakonda, kungakhale kovuta kuti iwo akhulupililile kuti Yehova amaŵakonda.

Tambitsani VIDIYO yakuti Tapeza Cikondi Cacikhristu m’Banja la Yehova. Kenako, funsani omvela kuti:

Kodi mwaphunzila ciyani kwa Lei Lei na Mimi pa nkhani yoonetsa ena cikondi?

Kodi tingacite ciyani pothandiza alambili anzathu kumva kuti Yehova amaŵakonda?

  • Muziŵaona kuti ni nkhosa za Yehova zamtengo wapatali.—Sal. 100:3

  • Kambani nawo mowalimbikitsa.—Aef. 4:29

  • Citani nawo mwacikondi.—Mat. 7:​11, 12

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 126 na Pemphelo