Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

January 8-14

YOBU 34-35

January 8-14

Nyimbo 30 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Ngati Zinthu Sizikukuyendelani pa Umoyo

(Mph. 10)

Kumbukilani kuti Yehova si ndiye amacititsa zopanda cilungamo (Yobu 34:10; wp19.1 8 ¶2)

Zingaoneke ngati anthu ambili salandila cilango pa zoipa zimene amacita, komabe sangathaŵe ciweluzo ca Yehova (Yobu 34:​21-26; w17.04 10 ¶5)

Njila yabwino yothandizila ocitidwa zopanda cilungamo ni kuwaphunzitsa za Yehova (Yobu 35:​9, 10; Mat. 28:​19, 20; w21.05 7 ¶19-20)

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Yobu 35:7—Kodi Elihu anatanthauzanji pofunsa Yobu kuti: “Kodi [Mulungu] amalandila ciyani kucokela m’manja mwanu?” (w17.04 29 ¶3)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zomwe mungakonde kutigaŵilako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Yobu 35:​1-16 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) NYUMBA NA NYUMBA. M’pempheni kuti muyambe kuphunzila naye Baibo. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Onetsani munthu amene ali ni ana aang’ono mmene angapezele nkhani zothandiza makolo pa jw.org. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 58

7. Kodi Mumalakalaka “Kulalikila Mawu” Mwamwayi?

(Mph. 15) Kukambilana.

Paulo analimbikitsa Timoteyo kuti: “Lalikila mawu. Lalikila modzipeleka.” (2 Tim 4:2) Liwu lacigiriki (velebu) lomasulidwa kuti “lalikila modzipeleka,” nthawi zina anali kulichula pokamba za msilikali kapena mlonda amene nthawi zonse anali kukhala cile kuti acitepo kanthu. Mawuwa amafotokoza bwino mmene timakhalila cile nthawi zonse kuti tipeze mpata woloŵetsapo ulaliki pa makambilano.

Cifukwa timamukonda Yehova ndipo timayamikila zonse zimene amaticitila, timafuna kuuzako ena za makhalidwe ake abwino.

Ŵelengani Salimo 71:8. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi ni zabwino ziti zokhudza Yehova zimene mumakonda kuuzako ena?

Cikondi cathu pa anthu cimatilimbikitsa kulalikila mwa mwayi.

Tambitsani VIDIYO yakuti Mmene Anthu Ofika M’mahandiledi Anaphunzilila Coonadi. Kenako funsani omvela kuti:

  •   Kodi ulaliki wamwayi unathandiza bwanji kuti anthu ofika m’mahandiledi apeze coonadi ca m’Baibo?

  •   Kodi anthu omwe poyamba anali acipembedzo cina anapindula bwanji atalandila coonadi?

  • Kodi kukonda anthu kumatilimbikitsa bwanji kucita ulaliki wamwayi?

  • Muona kuti n’cifukwa ciyani ulaliki wamwayi ni njila yabwino kwambili yothandizila anthu kudziŵa Yehova?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 138 na Pemphelo