Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

January 6-12

MASALIMO 127-134

January 6-12

Nyimbo 134 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Makolo, Pitilizani Kusamalila Colowa Canu ca Mtengo Wapatali

(Mph. 10)

Yehova angawathandize makolo kupeza zosoŵa za banja lawo (Sal. 127:​1, 2)

Ana ni mphatso ya mtengo wapatali yocokela kwa Yehova (Sal. 127:3; w21.08 5 ¶9)

Phunzitsani mwana aliyense malinga na zosoŵa zake (Sal. 127:4; w19.12 27 ¶20)

Yehova amasangalala kwambili makolo akamamudalila na kucita zonse zotheka posamalila ana awo

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 128:3​—N’cifukwa ciyani wamasalimo anakamba kuti ana ali ngati mphukila za mtengo wa maolivi? (it-1-E 543)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 132:​1-18 (th phunzilo 2)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Munthu waonetsa kuti amakhulupilila zosiyana ndi zimene Baibo imaphunzitsa. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)

6. Kupanga Ophunzila

(Mph. 5) lff phunzilo 16 mfundo 4-5. Kambilanani makonzedwe amene mwapanga kuti wophunzila wanu akaphunzilebe ngakhale kuti mudzacokapo. (lmd phunzilo 10 mfundo 4)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 13

7. Makolo, Kodi Mumagwilitsa Nchito Cida Camphamvu Ici Pophunzitsa Ana Anu?

(Mph. 15) Kukambilana.

Gulu la Yehova latulutsa zida zambili pothandiza makolo kuphunzitsa ana awo za Yehova. Komabe, cimodzi mwa zida zamphamvu kwambili cimene makolo ali naco ni citsanzo cawo cabwino.​—Deut. 6:​5-9.

Yesu anaseŵenzetsa cida camphamvu cimeneci pophunzitsa ophunzila ake.

Ŵelengani Yohane 13:​13-15. Kenako funsani omvela kuti:

  • Muganiza n’cifukwa ciyani njila ya Yesu yogwilitsa nchito citsanzo cake pophunzitsa inali yothandiza?

Inu makolo, citsanzo canu cimaonetsa ana anu kuti zimene mumawauza n’zothandizadi. Mukamaonetsa citsanzo cabwino kwa ana anu mudzawathandiza kuti azimvela zimene mumawaphunzitsa.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Kuphunzitsa Ana Athu Mwa Citsanzo. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi ni maphunzilo ofunika ati amene M’bale na Mlongo Garcia anaphunzitsa ana awo?

  • Kodi vidiyo iyi yakulimbikitsani bwanji kukhala citsanzo cabwino kwa ana anu?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 20 ¶13-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 73 na Pemphelo