Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

February 10-16

MASALIMO 147-150

February 10-16

Nyimbo 12 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Tili na Zifukwa Zambili Zotamandila Ya

(Mph. 10)

Amatisamalila aliyense payekha-payekha (Sal. 147:​3, 4; w17.07 18 ¶5-6)

Amamvetsa mmene timamvela ndipo amaseŵenzetsa mphamvu zake potithandiza (Sal. 147:5; w17.07 18 ¶7)

Watipatsa mwayi wapadela wokhala pakati pa anthu ake (Sal. 147:​19, 20; w17.07 21 ¶18)


DZIFUNSENI KUTI, ‘N’ciyaninso cina cimene cimanilimbikitsa kutamanda Yehova?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 148:​1, 10​—Kodi “mbalame zamapiko” zimatamanda Yehova m’njila yotani? (it-1-E 316)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 148:1–149:9 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KU NYUMBA NA NYUMBA. Munthu wakuuzani kuti ali na matenda aakulu. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pezani njila youzilako munthu zimene munaphunzila pa msonkhano waposacedwa. (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) w19.03 10 ¶7-11​—Mutu: Mvelani Yesu mwa Kulalikila Uthenga Wabwino. Onani cithunzi. (th phunzilo 14)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 159

7. Lipoti la Caka ca Utumiki

(Mph. 15) Kukambilana.

Pambuyo poŵelenga cilengezo cocokela ku ofesi ya nthambi cokhudza lipoti la caka ca utumiki, pemphani omvela kuti achuleko zina mwa zinthu zocititsa cidwi za mu Lipoti la Caka ca Utumiki ca 2024 la Mboni za Yehova pa Dziko Lonse. Funsani mafunso ofalitsa amene munawakonzekeletsa pasadakhale kuti asimbe zocitika zolimbikitsa za mu ulaliki za m’caka ca utumiki capita.

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 37 na Pemphelo