Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

February 24–March 2

MIYAMBO 2

February 24–March 2

Nyimbo 35 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. N’cifukwa Ciyani Muyenela Kuyikilapo Mtima pa Phunzilo la Inu Mwini?

(Mph. 10)

Kuti muonetse kuti mumayamikila coonadi (Miy. 2:​3, 4; w22.08 18 ¶16)

Kuti muzipanga zisankho zabwino (Miy. 2:​5-7; w22.10 19 ¶3-4)

Kuti mulimbitse cikhulupililo canu (Miy. 2:​11, 12; w16.09 23 ¶2-3)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ningacite ciyani kuti phunzilo langa la munthu mwini lizikhala lokhazikika komanso lopindulitsa kwambili?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Miy. 2:7​—Kodi ni motani mmene Yehova alili “cishango kwa anthu amene amacita zinthu mokhulupilika”? (it-1-E 1211 ¶4)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Miy. 2:​1-22 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) KU NYUMBA NA NYUMBA. Onetsani munthu mmene angapezele nkhani zopezeka pa jw.org zothandiza okwatilana. (lmd phunzilo 1 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Gaŵilani magazini yokhala na nkhani imene mwininyumba anacita nayo cidwi pa ulendo wapita. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Nkhani

(Mph. 5) lmd Zakumapeto A mfundo 8​—Mutu: Mwamuna na Mkazi Wake Akhale Okhulupilika kwa Wina na Mnzake. (th phunzilo 13)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 96

7. Kodi Mumakonda Kufufuza?

(Mph. 15) Kukambilana.

Inu acinyamata, kodi mungakonde kufufuza cuma cobisika? Ngati n’telo, dziŵani kuti m’Baibo muli cuma camtengo wapatali kwambili kuposa cina ciliconse. Cumaco ni kudziŵa Mulungu! (Miy. 2:​4, 5) Mungapeze cuma cimeneco mwa kupatula nthawi yoŵelenga Baibo nthawi zonse komanso kufufuza nkhani zimene mwaŵelengazo. Kucita zimenezi kungakhale kosangalatsa komanso kopindulitsa!

  • Kodi mungadzifunse mafunso ati poŵelenga Baibo? (w24.02 32 ¶2-3)

  • Kodi ni zida ziti zimene mungaseŵenzetse kuti mupeze mayankho?

Mavidiyo akuti Phunzilani kwa Mabwenzi a Yehova angakuthandizeni kudziŵa zimene mungacite posinkhasinkha zimene mwaŵelenga m’Baibo.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Phunzilani kwa Mabwenzi a Yehova​—Abele.

Ŵelengani Genesis 4:​2-4 komanso Aheberi 11:4. Kenako funsani omvetsela kuti:

  • Kodi Abele anaonetsa bwanji kuti anali bwenzi la Yehova?

  • Kodi Abele anacita ciyani kuti alimbitse cikhulupililo cake mwa Yehova?

  • Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 102 na Pemphelo