Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

February 3-9

MASALIMO 144-146

February 3-9

Nyimbo 145 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Osangalala Ndi Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova!”

(Mph. 10)

Yehova amadalitsa anthu amene amamudalila (Sal. 144:​11-15; w18.04 32 ¶3-4)

Timasangalala cifukwa ca ciyembekezo cathu (Sal. 146:5; w22.10 28 ¶16-17)

Anthu amene Mulungu wawo ni Yehova adzasangalala kwamuyaya (Sal. 146:10; w18.01 26 ¶19-20)

Tikamatumikila Yehova mokhulupilika, tingakhale osangalala ngakhale kuti tikukumana na mavuto

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 145:​15, 16​—Malinga na mavesiwa, kodi tiyenela kucita nazo motani nyama? (it-1-E 111 ¶9)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 144:​1-15 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) KU NYUMBA NA NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti akucita maphunzilo a ku yunivesite. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Seŵenzetsani vidiyo ya mu Thuboksi Yophunzitsila. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

6. Nkhani

(Mph. 4) lmd Zakumapeto A mfundo 7​—Mutu: Mkazi Azicitila Mwamuna Wake Ulemu Waukulu. (th phunzilo 1)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 59

7. Yehova Amafuna Kuti Mukhale Osangalala

(Mph. 10) Kukambilana.

Yehova ni Mulungu wacimwemwe. (1 Tim. 1:11) Watipatsa mphatso zambili zabwino zoonetsa kukula kwa cikondi cake pa ife komanso kuti amafuna tizisangalala. (Mlal. 3:​12, 13) Ganizilani mphatso ziŵili izi: Cakudya ndi luso la kumva.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Cilengedwe Cimaonetsa Kuti Yehova Amafuna Kuti Tizikondwela​—Zakudya Zokoma na Mamvekedwe Okoma Kumvetsela. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mphatso ziŵili izi, cakudya na luso la kumva, zimakutsimikizilani bwanji kuti Yehova amafuna kuti muzikhala osangalala?

Ŵelengani Salimo 32:8. Ndiyeno funsani omvela kuti:

  • Kodi kudziwa kuti Yehova amafuna kuti mukhale osangalala kumakulimbikitsani bwanji kutsatila malangizo ake opezeka m’Baibo komanso opelekedwa na gulu lake?

8. Zofunikila za Mpingo

(Mph. 5)

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 22 ¶1-6

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 85 na Pemphelo