January 20-26
MASALIMO 138-139
Nyimbo 93 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Musalole Mantha Kukulepheletsani Kutengako Mbali pa Misonkhano
(Mph. 10)
Timafuna kutamanda Yehova na mtima wathu wonse (Sal. 138:1)
Mukacita mantha pamene mukufuna kutengako mbali pa misonkhano, muzidalila Yehova kuti akuthandizeni (Sal. 138:3)
Kucita mantha kungaonetse kuti muli na khalidwe labwino (Sal. 138:6; w19.01 10 ¶10)
ZOYENELA KUCITA: Mayankho anu azikhala aafupi. Izi zidzakuthandizani kucepetsa mantha.—w23.04 21 ¶7.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Sal. 139:21, 22—Kodi Akhristu ayenela kukhululukila munthu aliyense? (it-1-E 862 ¶4)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 139:1-18 (th phunzilo 2)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)
5. Kupanga Ophunzila
(Mph. 4) ULALIKI WAPOYELA. M’pempheni kuti muziphunzila naye Baibo ndipo muonetseni mmene timacitila. (lmd phunzilo 10 mfundo 3)
6. Nkhani
(Mph. 5) ijwyp nkhani 105—Mutu: Mungatani Kuti Musamacite Manyazi Kwambili? (th phunzilo 16)
Nyimbo 59
7. Mungapambane mu Utumiki Wanu Ngakhale Kuti Ndinu Wamanyazi
(Mph. 15) Kukambilana.
Kodi ndinu wamanyazi? Kodi mumafuna kuti ena asakuoneni? Kodi mumacita mantha mukangoganizila zokambilana na anthu ena? Nthawi zina, manyazi angatilepheletse kucita zinthu zimene tingafune kucita. Komabe, ambili amene anali na vuto la manyazi akwanitsa kuuzako ena za Baibo na kupeza cimwemwe pa utumiki wawo. Ndiye tingaphunzile ciyani ku citsanzo cawo?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Nimatumikila na Mtima Wonse Ngakhale Kuti Ndine Wamanyazi. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi Mlongo Lee anapindula bwanji cifukwa cotsatila malangizo a agogo ake akuti ayenela “kutumikila Yehova na mtima wonse”?
Baibo imaonetsa kuti Mose, Yeremiya na Timoteyo ayenela kuti anali amanyazi. (Eks. 3:11; 4:10; Yer. 1:6-8; 1 Tim. 4:12) Komabe, iwo anakwanitsa kucita zinthu zazikulu potumikila Yehova cifukwa iye anali nawo. (Eks. 4:12; Yer. 20:11; 2 Tim. 1:6-8)
Ŵelengani Yesaya 43:1, 2. Kenako funsani omvela kuti:
-
Kodi Yehova anawalonjeza ciyani alambili ake?
Kodi Yehova angawathandize bwanji anthu amanyazi kuti apambane mu utumiki wawo?
Tambitsani VIDIYO YAKUTI Mmene Ubatizo Wanu Ungakubweletseleni Cimwemwe Cacikulu—Mbali Yake. Ndiyeno funsani omvela kuti:
-
Pa utumiki wake, kodi Mlongo Jackson anaiona motani thandizo Yehova?
-
Kodi utumiki ungamuthandize motani munthu wamanyazi?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 21 ¶8-13, bokosi pa tsa. 169