Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

January 27–February 2

MASALIMO 140-143

January 27–February 2

Nyimbo 44 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Muzicitapo Kanthu pa Zimene Mwapempha

(Mph. 10)

Muzikhala okonzeka kulandila malangizo kapena uphungu (Sal. 141:5; w22.02 12 ¶13-14)

Muzisinkhasinkha mmene Yehova anakuthandizilani komanso mmene anathandizila anthu ake (Sal. 143:5; w10 3/15 32 ¶4)

Muziyesetsa kuona zinthu mmene Yehova amazionela (Sal. 143:10; w15 3/15 32 ¶2)

Mu Masalimo 140-143 muli zimene Davide anapempha komanso zimene anacitapo pa mapemphelo ake.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 140:3​—N’cifukwa ciyani Davide anati lilime la anthu oipa lili ngati la njoka? (it-2-E 1151)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 141:​1-10 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Kambilanani na munthu pambuyo pomuthandiza zina zake. (lmd phunzilo 3 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Munthuyo wakuuzani kuti ni wotangwanika. (lmd phunzilo 7 mfundo 3)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Citsanzo. ijwfq nkhani 21​—Mutu: N’chifukwa Chiyani Mumakana Kuikidwa Magazi? (th phunzilo 7)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 141

7. Konzekelani Pali Pano Musanafunikile Cithandizo ca Mankhwala Kapena Opaleshoni

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova analonjeza kuti adzakhala “thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.” (Sal. 46:1) Zimabweletsa nkhawa mukafunikila cithandizo ca mankhwala kapena opaleshoni. Komabe, Yehova watipatsa zonse zofunikila potikonzekeletsa. Mwacitsanzo, gulu lake latipatsa khadi lopatsa munthu mphamvu yosasinthika yodzisankhila thandizo la mankhwala (DPA), Khadi ya Mwana, a komanso mafomu ena ofotokoza za cithandizo cacipatala. b Tilinso na Makomiti Okambilana ndi Acipatala (HLC). Zonsezi zimatithandiza kumvela lamulo la Mulungu pa nkhani ya magazi.​—Mac. 15:​28, 29.

Tambitsani VIDIYO YAKUTI Kodi Mwaikonzekela Mikhalidwe Yofuna Cithandizo Camankhwala? Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi kudzadza fomu ya DPA kwawathandiza bwanji ena?

  • Kodi fomu yakuti Mfundo Zokhudza Azimayi a Pathupi (S-401) yawathandiza bwanji ena?

  • N’cifukwa ciyani n’canzelu kudziŵitsa a HLC mwamsanga ngati mwadziŵa kuti adzakucitani adimiti, opaleshoni, kapena kukupatsani cithandizo cina ca mankhwala, monga ca matenda a khansa, ngakhale mutaona kuti sadzafunika kukuikani magazi?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 21 ¶14-22

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 103 na Pemphelo

a Ofalitsa obatizika angatenge khadi lawo la DPA komanso kutengela ana awo Khadi la Mwana kwa mtumiki wa mabuku.

b Pakakhala pofunikila, pemphani akulu kuti akupatseni mafomu awa, Mfundo Zokhudza Azimayi a Pathupi (S-401), Malangizo kwa Odwala Ofunikila Opaleshoni Kapena Cithandizo ca Kemofelapi (S-407), komanso Information for Parents Whose Child Requires Medical Treatment (S-55).