July 4- 10
Masalimo 60-68
Nyimbo 104 na Pemphelo
Mau Oyamba (Mph. 3 kapena zocepelapo)
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Tamandani Yehova Wakumva Pemphelo”: (Mph. 10)
Sal. 61:1, 8—Zimene timalonjeza Yehova, tizizichula m’mapemphelo athu (w99 9/15-CN, tsa. 9 ndime 1-4)
Sal. 62:8—Onetsani kuti mumam’dalila Yehova mwa kumukhutulila nkhawa zanu zonse popemphela (w15 4/15, masa. 25-26 ndime 6-9)
Sal. 65:1, 2—Yehova amamvela mapemphelo a anthu a maganizo oyenela (w15 4/15 22 ndime 13-14; w10 4/15-CN, tsa. 5 ndime 10; it-2 tsa, 668 ndime 2 E)
Kufufuza Cuma ca Kuuzimu: (Mph. 8)
Sal. 63:3—N’cifukwa ciani cifundo ca Yehova cimaposa moyo? (w06 6/1-CN, tsa. 11 ndime 7)
Sal. 68:18—N’ndani amene anali “mphatso za amuna”? (w06 6/1-CN, tsa. 10 ndime 5)
Kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno kwaniphunzitsa ciani za Yehova?
Ni mfundo ziti pa kuŵelenga Baibulo kwa mlungu uno zimene ningaseŵenzetse mu ulaliki?
Kuŵelenga Baibulo: (Mph. 4 kapena zocepelapo) Sal. 63:1–64:10
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Konzekelani Maulaliki a Mwezi Uno: (Mph. 15) Kukambilana. Tambitsani mavidiyo a ulaliki wa citsanzo, ndi kukambilana mfundo zake. Limbikitsani ofalitsa kukonza ulaliki wawo.
UMOYO WATHU WACIKHIRISTU
“Kukhala na Umoyo Wosafuna Zambili Kudzatithandiza Kutamanda Mulungu”: (Mph. 15) Yambani mwa kukamba nkhaniyi. Ndiyeno tambitsani ndi kukambilana mwacidule vidiyo yakuti Tili na Umoyo Wosafuna Zambili yopezeka pa JW Broadcasting. (Pitani polemba kuti VIDEO ON DEMAND > FAMILY.) Limbikitsani onse kuti aone mmene angakhalile na umoyo wosalila zambili n’colinga cakuti atumikile Yehova mokwanila.
Phunzilo la Baibulo la Mpingo: (Mph. 30) ia mutu 19 ndime 1-16
Kubwelelamo ndi Kuchulako za Mlungu Wotsatila (Mph. 3)
Nyimbo 88 na Pemphelo