Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Maulaliki a Citsanzo

Maulaliki a Citsanzo

NSANJA YA MLONDA

Funso: Anthu ayesapo kuwononga Baibulo, koma alephela. Kodi zimenezi si umboni woonetsa kuti Baibulo ni buku locokela kwa Mulungu?

Lemba: Yes. 40:8

Cogaŵila: Nkhani zotsatizana za m’magazini iyi, zifotokoza nkhani yocititsa cidwi ya mmene Baibulo yapulumukila.

NSANJA YA MLONDA (tsamba lothela)

Funso: Nifuna nimveleko maganizo anu pa funso ili. [Ŵelengani funso loyamba pa tsamba 16.] Anthu ena amakhulupilila kuti cipembedzo n’ca anthu cabe. Ndipo ena amaganiza kuti cipembedzo cimatithandiza kuyandikila Mulungu. Nanga inu muganiza bwanji?

Lemba: Yak. 1:27

Cogaŵila: Nkhani iyi ifotokoza zowonjezeleka zimene Baibulo imakamba. Kodi nikabwelenso kuti tikakambilane mfundo za m’nkhani imeneyi?

UTHENGA WABWINO WOCOKELA KWA MULUNGU

Funso: Anthu ambili amaŵelenga ulosi wa m’Baibulo mosasamala kwenikweni ngati kuti akuŵelenga nyuzipepala. N’zocitika ziti zimene Baibulo inakambilatu zimene mwaonapo kapena kumvelapo?

Lemba: 2 Tim. 3:1-5

Cogaŵila: Kabuku aka kaonetsa kuti mau awa ni uthenga wabwino kwa anthu okonda Mulungu. [Kambilanani phunzilo 1, funso 2.]

KONZANI ULALIKI WANU

Funso:

Lemba:

Cogaŵila: