UMOYO WATHU WACIKHRISTU
N’cifukwa Ciani Kusatengako Mbali Mundale N’kofunika? (Mika 4:2)
Fanizo la Msamariya wacifundo litikumbutsa kuti Yehova alibe tsankho, ndipo amafuna kuti ise ‘tizicitila onse zabwino,’ ngakhale anthu olemela kapena osauka, amene timasiyana nawo mtundu, cikhalidwe, kapena cipembedzo.—Agal. 6:10; Mac. 10:34.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI N’CIFUKWA CIANI KUSATENGAKO MBALI MUNDALE N’KOFUNIKA? (MIKA 4:2), NDIYENO YANKHANI MAFUNSO OTSATILA:
-
Tidziŵa bwanji kuti lemba la Mika 4:2 likamba zimene zikucitikila anthu a Mulungu masiku ano?
-
Kodi ucete n’ciani? Nanga n’cifukwa ciani ni wofunika?
-
Kodi Chivumbulutso 13:16, 17, ionetsa kuti ndale za dziko zimakhudza bwanji kaganizidwe kathu na zocita zathu?