Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 6-7

Tizipimila Ena Mowolowa Manja

Tizipimila Ena Mowolowa Manja

6:38

Munthu wowolowa manja amapeleka mokondwela nthawi yake, mphamvu zake, na zinthu zake kuti athandize ena na kuwalimbikitsa.

  • Mau a Cigiriki amene anawamasulila kuti “khalani opatsa” atanthauza kucita cinthu mosalekeza

  • Ngati tikhala opatsa, ena adzatikhuthulila m’matumba athu “muyezo wabwino, wotsendeleka, wokhuchumuka ndi wosefukila.” Mau amenewa angatanthauze cizoloŵezi ca ogulitsa malonda amene amaikapo mbasela pa zinthu zimene munthu wagula