Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU | LUKA 8-9

Khala Wotsatila Wanga—Motani?

Khala Wotsatila Wanga—Motani?

9:62

Kuti munthu wogwila pulawo asapange mizele yobenda, safunika kucenjenekewa na zimene wasiya m’mbuyo. Mofananamo, Mkhristu safunika kulola kuti zinthu zimene anasiya m’dzikoli zimucenjeneke.—Afil. 3:13.

Tikakumana na mavuto, zimakhala zosavuta kuyamba kulaka-laka zinthu monga ‘zimene tinali kucita kale’ tisaphunzile coonadi. Tikayamba kuzilaka-laka, timaganizila kwambili pa zimene zinali kutisangalatsa, n’kumacepetsa mavuto amene tinakumana nawo panthawiyo. Izi n’zimene Aisraeli anacita atacoka ku Iguputo. (Num. 11:5, 6) Ngati timakhala na maganizo aconco, tingayesedwe ndipo tingabwelele ku umoyo wathu wakale. Conco, tingacite bwino kuganizila madalitso amene tapeza palipano, na madalitso amene tidzapeza m’tsogolo mu Ufumu.—2 Akor. 4:16-18.