CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Afikeni Pamtima Anthu
Mtima ndiwo umasonkhezela munthu kumvela Mulungu. (Miy. 3:1) Conco pamene tikuphunzitsa munthu, tiyenela kuyesetsa kumufika pamtima. Motani?
Sitiyenela kungophunzitsa wophunzila mfundo za coonadi ca m’Baibo. Koma tiyenelanso kum’thandiza kuona mmene mfundozo zimakhudzila umoyo wake komanso ubale wake na Yehova. M’thandizeni kuona kuti miyezo ya m’Baibo imaonetsa cikondi ca Mulungu, ubwino wake, na cilungamo cake. M’funseni mafunso mwaluso komanso mokoma mtima kuti mum’thandize kupendanso bwino mmene amaonela mfundo zimene akuphunzila. M’thandizeni kuganizila mapindu amene adzapeza akasintha maganizo ake olakwika na zizoloŵezi zoipa. Mukaona kuti wophunzila wayamba kukonda Yehova na mtima wonse, cimwemwe canu cidzawonjezeka.
ONELELANI VIDYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUWAFIKA PAMTIMA ANTHU. KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
-
N’cifukwa ciani Neeta anafunsa Rose kuti: “Kodi unaiganizilaponso nkhani ija tinakambilana pa Mande?”
-
Kodi Neeta anamuthandiza bwanji Rose kuzindikila kuti miyezo ya m’Baibo imaonetsa kuti Yehova amamukonda?
-
Kodi Neeta anamuthandiza bwanji Rose kuganizila mmene angaonetsele kuti amakonda Mulungu?