UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kukhala Wolimba Mtima Sikovuta
Kulimba mtima kumatanthauza kuvala zilimbe, kapena kuti kukhala wolimba. Sikutanthauza kuti munthu alibiletu mantha. Koma kumatanthauza kusaopa kucita zinthu ngakhale kuti tili na mantha. Yehova ndiye Gwelo la kulimba mtima kweni-kweni. (Sal. 28:7) Kodi acinyamata angaonetse bwanji kulimba mtima?
ONELELANI VIDIYO YAKUTI TENGELANI CITSANZO CA ANTHU OLIMBA MTIMA, OSATI AMANTHA! PAMBUYO PAKE YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Ni zocitika ziti zofuna kulimba mtima zimene acinyamata amakumana nazo?
-
Ni nkhani ziti za m’Baibo zimene zimatisonkhezela kukhala olimba mtima?
-
Kodi ife na anthu otiona timapindula bwanji ngati ticita zinthu molimba mtima?