Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Akazi Acikulile Muzicita Nawo Zinthu Monga Amayi Anu, Akazi Acitsikana Monga Azilongosi Anu

Akazi Acikulile Muzicita Nawo Zinthu Monga Amayi Anu, Akazi Acitsikana Monga Azilongosi Anu

Malemba amatilimbikitsa kuti Akhristu acikulile tizicita nawo zinthu monga amayi athu kapena atate athu, Akhristu acinyamata monga alongosi athu kapena abale athu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:1, 2.) Abale maka-maka, ayenela kulemekeza alongo na kuwapatsa ulemu.

M’bale sayenela kuceza mokopana na mlongo amene si mkazi wake kapena kucita zinthu zimene zingapangitse mlongo kumangika thupi. (Yobu 31:1) M’bale amene ni mbeta sayenela kuseŵeletsa malingalilo a mlongo amene ni mbeta mwa kucita zinthu zoonetsa ngati kuti afuna kukhala naye pa cibwenzi, pamene m’ceni-ceni alibe colinga cimeneco.

Akulu mokoma mtima, ayenela kuganizila alongo amene afunsa funso mwaulemu kapena amene awafotokozela zina zake zofuna cisamalilo cawo. Akulu amadela nkhawa maka-maka alongo amene alibe amuna awo n’colinga cakuti awateteze.—Rute 2:8, 9.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI ONETSANI CIKONDI COSATHA MUMPINGO—KWA AKAZI AMASIYE NDI ANA AMASIYE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi mpingo unamuonetsa bwanji cikondi capadela Mlongo Myint?

  • Kodi cikondi cimene mpingo unaonetsa cinathandiza bwanji kucitila umboni wabwino m’mudzi wawo?

  • Kodi cikondi cimene mpingo unaonetsa cinawathandiza bwanji ana a Mlongo Myint?

Kodi mungaonetse m’njila ziti kuti alongo mumawadela nkhawa mwacikondi mumpingo wanu?