UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Musamade Nkhawa”
Yehova anali kuthandiza anthu osauka mu Isiraeli wakale. Kodi n’ziti zina zimene wacita pothandiza atumiki ake osauka masiku ano?
-
Anawaphunzitsa kuona ndalama moyenela.—Luka 12:15; 1 Tim. 6:6-8
-
Amawathandiza kudziona kuti ni ofunika.—Yobu 34:19
-
Anawaphunzitsa kugwila nchito molimbika na kupewa zizoloŵezi zoipa.—Miy. 14:23; 20:1; 2 Akor. 7:1
-
Anawabweletsa m’gulu lacikondi la abale acikhristu.—Yoh. 13:35; 1 Yoh. 3:17, 18
-
Anawapatsa ciyembekezo.—Sal. 9:18; Yes. 65:21-23
Olo zinthu zivute bwanji pa umoyo, sitiyenela kuda nkhawa. (Yes. 30:15) Yehova adzatithandiza kupeza zofunikila zakuthupi, malinga ngati tipitiliza kufuna-funa ufumu wake coyamba.—Mat. 6:31-33.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI CIKONDI SICITHA OLO KUTI. . . NDIMWE OSAUKA—CONGO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi abale amene amakhala kufupi na malo ocitilako msonkhano wacigawo, amaonetsa bwanji mzimu woceleza kwa abale ocokela kutali obwela ku msonkhano?
-
Kodi vidiyo imeneyi itiphunzitsa ciani za cikondi ca Yehova pa osauka?
-
Kaya ndife olemela kapena osauka, tingatengele bwanji citsanzo ca Yehova?