CITANI KHAMA PA ULALIKI | WONJEZELANI CIMWEMWE CANU MU ULALIKI
Onetsani Cifundo
Cifundo cimatanthauza kumvetsetsa mmene ena amaganizila, mmene amamvelela, zimene amakonda, na zimene amafunikila. N’zosavuta anthu ena kudziŵa ngati timawamvela cifundo. Mtima wofunadi kuthandiza ena ndiwo umatisonkhezela kuwaonetsa cifundo. Tikamaonetsa cifundo mu ulaliki, timatengela khalidwe la Yehova la cikondi komanso lodela nkhawa ena, ndipo izi zimawasonkhezela kufuna kuphunzila za iye.—Afil. 2:4.
Tisamaonetse cifundo na colinga cofuna cabe kuphunzitsa munthu. Timaonetsa cifundo mwa kumumvetsela munthu mosamala komanso mokoma mtima. Timaonetsanso cifundo mwa zokamba zathu, khalidwe lathu, magesica amene timacita, komanso mmene nkhope yathu ionekela. Timasonyeza cifundo mwa kumuonetsa cidwi ceni-ceni munthu. Timaganizila zimene amakonda, zimene amakhulupilila komanso mmene zinthu zilili pa umoyo wake. Timaphunzitsa anthu mfundo zothandiza na kuwapatsa thandizo lofunikila, koma sitiwakakamiza kusintha umoyo wawo. Ngati ena alandila thandizo limene tawapatsa, cimwemwe cathu mu ulaliki cimawonjezeka.
ONELELANI VIDIYO YAKUTI PEZANI CIMWEMWE PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA—NOLANI MALUSO ANU—KUONETSA CIFUNDO, NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anacedwa?
-
Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anakamba kuti sakanakwanitsa kuphunzila cifukwa colema?
-
Kodi Neeta anaonetsa bwanji cifundo pamene Rose anakamba kuti alibe dongosolo kweni-kweni?