UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kampeni Yapadela Yoyambitsa Maphunzilo a Baibo mu September
Mu September, tidzayesetsa kupempha mwininyumba aliyense kuti tiziphunzila naye Baibo poseŵenzetsa kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! M’mweziwu, ofalitsa adzakhala na mwayi wosankha kucita upainiya wothandiza wa maola 30. Kodi tidzacita bwanji kampeni yapadela imeneyi?
-
Pa Ulendo Woyamba: Seŵenzetsani mfundo za pa cikuto cakumbuyo ca kabukuka pokopa cidwi ca munthu, ndipo m’pempheni kuti mumuonetse mmene phunzilo la Baibo limacitikila. Musaiŵale anthu amene anaonetsa cidwi kumbuyoko, kuphatikizapo amene mumacitako maulendo obwelelako. Ngakhale amene kale anali kukana kuphunzila Baibo, mwina angakhale na cidwi na njila yatsopano yophunzilila komanso kabuku katsopano. Simuyenela kusiya tumabuku tumenetu pa nyumba zimene simunapezepo anthu. Komanso musatumize tumabukutu m’makalata amene mwalembela anthu omwe sanaonetsepo cidwi. M’mwezi umenewu, Komiti ya Utumiki ya Mpingo ingawonjezele masiku ena okumana kaamba kotenga malangizo a ulaliki.
-
Mipata Ina: Ngati mpingo wanu umaseŵenzetsa tumasitandi twa ulaliki, muyenela kuonetsa cithunzi ca kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya pa tumasitandito. Munthu akaonetsa cidwi, muuzeni kuti akalandila kabuku kameneka, alinso na mwayi wolandila maphunzilo a Baibo aulele. Kenako muonetseni mwacidule mmene phunzilo la Baibo limacitikila, kapena panganani naye kuti mukamuonetse panthawi ina. Woyang’anila utumiki angapange makonzedwe akuti ofalitsa aluso akalalikile m’gawo lamalonda, na kupempha anthu kuti ayambe kuphunzila nawo Baibo. Mungapemphenso anzanu a kunchito, kapena amene mwakumana nawo pocita ulaliki wamwayi kuti muyambe kuphunzila nawo Baibo.
Yesu anatilamula kupanga ophunzila na ‘kuwaphunzitsa.’ (Mat. 28:19, 20) Pemphelo lathu n’lakuti kampeni yapadelayi itithandize kukwanilitsa udindo umenewu pogwilitsila nchito cofalitsa cimeneci cakuti Kondelani na Moyo Kwamuyaya!