UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kodi Mumayesetsa Kuona Mmene Yehova Amayankhila Mapemphelo Anu?
M’Baibo muli zitsanzo zambili za mapemphelo amene Yehova anayankha. Pamene atumiki a Mulungu anaona kuti iye wamva nkhawa zawo na kuwathandiza, mosakayikila cikhulupililo cawo cinalimba. Cotelo, ni bwino kuti popeleka mapemphelo athu, tizichula zinthu mosapita m’mbali na kuyesetsa kuona mmene Yehova watiyankhila. Komabe, tiyenela kukumbukila kuti yankho la Yehova lingakhale losiyana na zimene tinapempha, kapena angaticitile zambili kuposa zimene tinapempha. (2 Akor. 12:7-9; Aef. 3:20) Kodi Yehova angacite ciyani poyankha mapemphelo athu?
-
Angatipatse mphamvu, kutitonthoza, na kulimbitsa cikhulupililo cathu kuti tikwanitse kupilila mavuto amene takumana nawo. —Afil. 4:13
-
Angatipatse nzelu kuti tikwanitse kupanga zisankho zabwino.—Yak. 1:5
-
Angalimbitse zokhumba zathu na kutipatsa mphamvu kuti ticitepo kanthu.—Afil. 2:13
-
Angatithandize kukhala osatekeseka pamene tili na nkhawa.—Afil. 4:6, 7
-
Angasonkhezele ena kuti atithandize pa zosowa zathu kapena kutilimbikitsa.—1 Yoh. 3:17, 18
-
Angapeleke thandizo kwa anthu amene timawapemphelela.—Mac. 12:5, 11
ONELELANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA NI “WAKUMVA PEMPHELO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi nkhani ya M’bale Shimizu ingatilimbikitse bwanji ngati timalephela kucita zambili cifukwa ca matenda?
-
Tingatengele bwanji citsanzo ca M’bale Shimizu?