August 8-14
1 MAFUMU 3-4
Nyimbo 88 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Phindu la Nzelu”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
1 Maf. 4:20—Kodi n’ciyani cocititsa cidwi na mawu akuti “kuculuka kwake anali ngati mcenga wa m’mphepete mwa nyanja”? (w98 2/1 11 ¶15)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 1 Maf. 3:1-14 (th phunzilo 5)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. M’fotokozeleni mmene phunzilo la Baibo limacitikila, na kum’patsa kakhadi kofunsila phunzilo la Baibo. (th phunzilo 1)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Makambilano anu atsamile pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. M’gaŵileni kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya, na kuchulako za vidiyo yakuti Kodi Phunzilo la Baibulo Limacitika Bwanji? (koma musaitambitse) (th phunzilo 3)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 06 mfundo 4 (th phunzilo 12)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Zofunikila za Mpingo: (Mph. 10)
Dziikileni Zolinga za Caka ca Utumiki Catsopano—Muzipeleka Mowoloŵa Manja: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Loŵani pa Khomo la Zocita Zambili m’Cikhulupililo—“Ikani Kenakake Pambali” Kothandizila pa Nchito ya Yehova. Ndiyeno funsani omvela funso lakuti, Kodi banjali linaonetsa kuwoloŵa manja m’njila ziti?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 15, na mfundo ya kumapeto 2
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 14 na Pemphelo