July 25-31
2 SAMUELI 23-24
Nyimbo 76 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kodi Mumapeleka Nsembe Zanu Modzimana?”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
2 Sam. 23:15-17—N’cifukwa ciyani Davide anakana kumwa madzi amene asilikali ake anakam’tungila? (w05 5/15 19 ¶6)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 2 Sam. 23:1-12 (th phunzilo 11)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Yambitsani makambilano poseŵenzetsa mfundo za pacikuto cothela ca kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Panganani naye kuti ulendo wotsatila, mukayankhe funso lalikulu m’phunzilo 01, limenenso ni mutu wa phunzilolo. (th phunzilo 9)
Ulendo Wobwelelako: (Mph. 4) Kambilanani na munthu amene analandila kabuku kakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!, na kumuonetsa mmene phunzilo la Baibo limacitikila. (th phunzilo 3)
Phunzilo la Baibo: (Mph. 5) lff phunzilo 05 cidule cake, mafunso obweleza, na zocita (th phunzilo 19)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Pelekani Nsembe Mofunitsitsa (Sal. 54:6): (Mph. 9) Onetsani vidiyoyi.
Khala Bwenzi la Yehova—Kudzimana: (Mph. 6) Kukambilana. Onetsani vidiyoyi. Ndiyeno ngati n’kotheka, funsani mafunso ana amene munawasankhilatu. Afunseni kuti: Kodi Kalebe na Sofiya anacita ciyani poonetsa kudzimana? Kodi citsanzo ca Yesu cinam’thandiza bwanji Kalebe? Kodi inu mwadzimana zinthu zotani pofuna kukondweletsa Yehova na kuthandiza ena?
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 13, na mfundo ya kumapeto 1
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 32 na Pemphelo