July 4-10
2 SAMUELI 18-19
Nyimbo 138 na Pemphelo
Mawu Oyamba (Mph. 1)
CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Barizilai Ni Citsanzo ca Kudzicepetsa”: (Mph. 10)
Kufufuza Cuma Cauzimu: (Mph. 10)
2 Sam. 19:24-30—Kodi citsanzo ca Mefiboseti cingatilimbikitse bwanji? (w20.04 30 ¶19)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, ni mfundo yopindulitsa iti imene munapeza yokhudza Yehova, ulaliki, kapena mfundo ina iliyonse?
Kuŵelenga Baibo: (Mph. 4) 2 Sam. 19:31-43 (th phunzilo 2)
CITANI KHAMA PA ULALIKI
Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (Mph. 5) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Ulendo Woyamba: Colinga ca Mulungu—Gen. 1:28. Nthawi zonse vidiyo ikaima, inunso iimitseni na kufunsa omvela mafunso amene aonekela.
Ulendo Woyamba: (Mph. 3) Makambilano anu atsamile (azikidwe) pa mfundo yaikulu ya makambilano acitsanzo. Mukayamba kukambilana, mwininyumba akambe mawu ofala kwanuko ofuna kukanila ulaliki. * Koma mwaluso loŵelani pa mawu amenewo. (th phunzilo 1)
Nkhani: (Mph. 5) w21.08 23-25 ¶15-19—Mutu: Mungadziikile Zolinga Zotani Ngati Mikhalidwe Siikulolani Kucita Zambili? (th phunzilo 20)
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Dziikileni Zolinga za Caka ca Utumiki Catsopano—Kucita Upainiya”: (Mph. 15) Kukambilana. Onetsani vidiyo yakuti Khalani Olimba Mtima . . . Inu Apainiya.
Phunzilo la Baibo la Mpingo: (Mph. 30) lff phunzilo 11
Mawu Othela (Mph. 3)
Nyimbo 97 na Pemphelo
^ Onani nkhani imene ili pa tsamba 16.