Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe

Mungathandize Kuti m’Banja Lanu Mukhale Cimwemwe

Yehova amafuna kuti anthu m’banja azikhala acimwemwe. (Sal. 127:3-5; Mlal. 9:9; 11:9) Komabe, tingataye cimwemwe cathu cifukwa ca mavuto a m’dzikoli, komanso cifukwa ca zophophonya za a m’banja lathu. Kodi aliyense angacite ciyani kuti m’banja lawo mukhale cimwemwe?

Mwamuna ayenela kupatsa ulemu mkazi wake. (1 Pet. 3:7) Ayenela kumapeza nthawi yoceza naye. Asamamuyembekezele kucita zimene sangakwanitse, ndipo azionetsa kuti amayamikila zimene amamucitila komanso zimene amacitila banja lawo. (Akol. 3:15) Azimuonetsa cikondi na kum’tamanda.—Miy. 31:28, 31.

Mkazi ayenela kufuna-funa njila zothandizila mwamuna wake. (Miy. 31:12) Azigonjela mwamuna wake na kugwilizana naye pocita zinthu. (Akol. 3:18) Azikamba zabwino za iye na kulankhula naye mokoma mtima.—Miy. 31:26.

Makolo ayenela kumapatula nthawi yoceza na ana awo. (Deut. 6:6, 7) Komanso aziwauza kuti amawakonda. (Mat. 3:17) Ndipo powapatsa cilango, azicita nawo mwacikondi komanso mozindikila.—Aef. 6:4.

Ana ayenela kulemekeza makolo awo na kuwamvela. (Miy. 23:22) Azimasuka kufotokozela makolo awo zimene akuganiza komanso mmene akumvela. Azimvela uphungu na ulangizi wa makolo awo, ndipo azionetsa kuti amawalemekeza makolowo.—Miy. 19:20.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI KULITSANI CIMWEMWE M’BANJA LANU, KENAKO YANKHANI FUNSO ILI:

Kodi aliyense wa anthu a mu vidiyo imeneyi anacita ciyani kuti akulitse cimwemwe m’banja lawo?