Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Kampeni Yapadela Yolengeza Ufumu wa Mulungu mu September!

Kampeni Yapadela Yolengeza Ufumu wa Mulungu mu September!

M’mwezi wa September, tidzakhala na nchito yapadela yolengeza mwakhama za Ufumu wa Mulungu kuti ndiwo njila yokha yothetsela mavuto a anthu. (Mat. 24:14) Kodi mungatengeko mbali motani pa nchitoyi? Mukaŵelenge lemba lokamba za Ufumu wa Mulungu kwa anthu ambili mmene mungathele m’mwezi umenewo. Ngati winawake waonetsa cidwi, mugaŵileni Nsanja ya Mlonda yogaŵila ya Na. 2 2020. Mukatelo, mukabweleleko mwamsanga, ndipo mukayesetse kuyambitsa phunzilo la Baibo poseŵenzetsa bulosha yakuti Kondwelani na Moyo Kwamuyaya! Onse amene adzacita upainiya wothandiza mu September adzakhala na ufulu wolalikila maola 15 kapena 30.

Posacedwa, Ufumu wa Mulungu udzaphwanya maufumu onse otsutsana nawo. (Dan. 2:44; 1 Akor. 15:24, 25) Conco, tiyeni tiuseŵenzetse mokwanila mwayi wapadela umenewu, poonetsa kuti ndife okhulupilika kwa Yehova na Ufumu wake!