Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Khalani Wokhulupilika kwa Yehova Posankha Mabwenzi

Khalani Wokhulupilika kwa Yehova Posankha Mabwenzi

Aamoni na Amowabu sanali kuloledwa “kubwela mumpingo” wa Mulungu cifukwa kale anali kulimbana na anthu a Mulungu (Neh. 13:1, 2; it-1 95 ¶5)

Mkulu wa Ansembe Eliyasibu analola Mwamoni kugwilitsa nchito cipinda codyela ca m’kacisi (Neh. 13:4, 5; w13 8/1 9 ¶5-6)

Nehemiya anaonetsa kukhulupilika kwake kwa Yehova mwa kuthetsa mgwilizano umene Eliyasibu anapanga na mdani wa Mulungu (Neh. 13:7-9)

Kodi tingaonetse kuti ndife okhulupilika kwa Yehova ngati tisankha mabwenzi amene samukonda?—w96 3/15 16 ¶6.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi Yehova amamva bwanji poona mabwenzi amene nimasankha?’