Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Tengelani Cikondi Cosasintha ca Yehova

Tengelani Cikondi Cosasintha ca Yehova

Yehova ndiye citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yoonetsa cikondi cosasintha. (Sal. 103:11) Ici si cikondi ca kanthawi cabe. Cikondi cosasintha ni cikondi cacikulu komanso cokhalitsa. Yehova anaonetsa khalidwe limeneli kwa anthu ake Aisiraeli m’njila zambili. Anawamasula mu ukapolo ku Iguputo na kuwaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Sal. 105:42-44) Anali kuwamenyela nkhondo, ndipo mobweleza-bweleza anawakhululukila macimo awo. (Sal. 107:19, 20) ‘Tikamacita cidwi na nchito za Yehova’ zoonetsa cikondi cake cosasintha, timalimbikitsidwa kutengela citsanzo cake.—Sal. 107:43.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI GANIZILANI NCHITO ZA YEHOVA ZOONETSA CIKONDI CAKE COKHULUPILIKA,” NDIYENO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi tingaonetse cikondi cosasintha m’njila ziti?

  • N’cifukwa ciyani kuonetsa cikondi cosasintha kumafuna kudzimana?