Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Amagwila Nchito Molimbika Potitumikila

Amagwila Nchito Molimbika Potitumikila

Oyang’anila madela na akazi awo amaonetsa cikondi codzimana kwa abale na alongo amene amawatumikila. Mofanana na ife tonse, nawonso ali na zosoŵa zawo. Ndipo nthawi zina amalema, amalefuka, ndiponso amakhala na nkhawa. (Yak. 5:17) Ngakhale n’conco, mlungu uliwonse iwo amayesetsa kulimbikitsa abale na alongo a mumpingo umene akuucezela. Kukamba zoona, oyang’anila madela “ayenela kupatsidwa ulemu waukulu.”—1 Tim. 5:17.

Pamene mtumwi Paulo anali kukonzekela zopita ku Roma kukagaŵila mpingo wa kumeneko “mphatso inayake yauzimu”, anali kuyembekezela ‘kukalimbikitsana’ na abale na alongo. (Aroma 1:11, 12) Kodi muganiza kuti mungamulimbikitse bwanji woyang’anila dela wanu na mkazi wake, ngati ni wokwatila?

ONELELANI VIDIYO YAKUTI UMOYO WA OYANG’ANILA DELA AMENE AMATUMIKILA KU MIDZI, KENAKO KAMBILANANI MAFUNSO AWA:

  • Kodi oyang’anila madela na akazi awo amaonetsa bwanji cikondi codzimana potumikila mipingo?

  • Kodi inu pacanu mwapindula bwanji na khama lawo?

  • Kodi mungawalimbikitse bwanji?