Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Zotulukapo Zowawa za Kusamvela

Zotulukapo Zowawa za Kusamvela

Aisiraeli ena anapanga mgwilizano wa ukwati na anthu olambila mafano (Ezara 9:1, 2; w06 1/15 20 ¶1)

Iwo ananyalanyaza malamulo omveka bwino a Yehova (Ezara 9:10-12)

Kusamvela kwawo kunabweletsa mavuto aakulu pa iwo na mabanja awo (Ezara 10:10, 11, 44)

Lamulo lililonse la Yehova limatipindulila. (w09 10/1 10 ¶6) Kumvela kudzatiteteza ku mavuto pali pano, komanso kudzathandiza kuti tikalandile madalitso osatha kutsogolo.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kumvela Yehova kwaniteteza bwanji ku mavuto?’