UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Kuteteza ndi Kukhazikitsa Mwalamulo” Nchito ya Uthenga Wabwino
Pamene otsutsa anayesa kuletsa Aisiraeli kumanga kacisi, omangawo anacita zonse zotheka kuti mwalamulo akhale na ufulu wopitiliza kumanga. (Ezara 5:11-16) Mofananamo, masiku ano Akhristu amacita zonse zotheka kuti akhalile kumbuyo nchito ya uthenga wabwino na kuikhazikitsa mwalamulo. (Afil. 1:7) Kuti izi zitheke, Dipatimenti ya Zamalamulo inakhazikitsidwa ku likulu mu 1936. Masiku ano, Dipatimenti ya Zamalamulo ku Likulu ndiyo imayang’anila nchito yoteteza mwalamulo zinthu za Ufumu padziko lonse. Kodi dipatimentiyi yathandiza bwanji pa nchito ya Ufumu? Nanga yawapindulila bwanji anthu a Mulungu?
ONELELANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE DIPATIMENTI YA ZAMALAMULO KU LIKULU IMACITA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:
-
Kodi ni mavuto otani okhudza za malamulo amene Mboni za Yehova zakumanapo nawo?
-
Kodi tinapambanapo milandu iti? Pelekani citsanzo
-
Nanga n’ciyani cimene aliyense wa ife angacite pothandiza “kuteteza ndi kukhazikitsa mwalamulo” uthenga wabwino?
-
Pa webusaiti yathu, ni pa mbali iti maka-maka pamene tingapezepo nkhani za malamulo zokhudza anthu a Mulungu, komanso maina a Mboni za Yehova zimene zili m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo?