CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Musalowelele Nchito Yomanga Nyumba ya Mulungu”
Mkulu wa Ansembe Yesuwa (Yoswa) na Bwanamkubwa Zerubabele anatsogolela pa nchito yomanganso kacisi, ngakhale kuti nchitoyo inali yoletsedwa (Ezara 5:1, 2; w22.03 18 ¶13)
Pamene otsutsa anafunsa Ayuda kuti ndani anawavomeleza kumanga, iwo anafotokoza za lamulo la Koresi (Ezara 5:3, 17; w86 2/1 29, bokosi ¶2-3)
Mfumuyo inatsimikizila za lamulo loyamba lija, ndiponso inalamula otsutsawo kuti aleke kuloŵelela pa nchito yomangayo (Ezara 6:7, 8; w22.03 15 ¶7)
ZOYENELA KUSINKHASINKHA: Kodi nkhani ya m’Baibo imeneyi itilimbikitsa bwanji kutsatila malangizo a anthu oikidwa na Yehova kuti azititsogolela, ngakhale kuti malangizowo sitikuwamvetsa?—w22.03 19 ¶16.