CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Kodi Mumaona Kuti Nchito Yamanja si Yokuyenelelani?
Mkulu wa ansembe na abale ake sanadzione kuti anali apamwamba kwambili moti n’kulephela kumanga nawo mpanda wa Yerusalemu (Neh. 3:1)
Amuna ena otchuka sanadzicepetse kuti agwile nawo nchito yomanganso mpanda (Neh. 3:5; w06 2/1 10 ¶1)
Akazi oopa Mulungu anagwila nawo na mtima wonse nchito yolemetsa imeneyo (Neh. 3:12; w19.10 23 ¶11)
Nchito zambili zimene zimacitika mumpingo ni zamanja komanso zooneka ngati zapansi, ndipo nthawi zina ena sangaone nchitozo.—w04 8/1 18 ¶16.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi kugwila nchito zooneka ngati zapansi cifukwa ca uthenga wabwino nimakuona bwanji?’—1 Akor. 9:23.