August 19-25
MASALIMO 75-77
Nyimbo 120 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. N’cifukwa Ciyani Simuyenela Kudzitukumula?
(Mph. 10)
Anthu odzitukumula sakondweletsa Mulungu (Sal. 75:4; 1 Tim. 3:6; w18.01 28 ¶4-5)
Udindo kapena utumiki uliwonse umene tingapatsidwe mu mpingo ni mphatso yocokela kwa Yehova ndipo sizidalila pa luso lathu (Sal. 75:5-7; w06-CN 7/15 11 ¶3)
Anthu onyada, monga olamulila a dziko odzitukumula, Yehova adzawacititsa manyazi (Sal. 76:12)
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 76:10—Kodi “mkwiyo wa munthu” ungatamande bwanji Yehova? (w06-CN 7/15 11 ¶4)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 75:1–76:12 (th phunzilo 11)
4. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Tambitsani vidiyo ya pa jw.org m’cinenelo cimene munthuyo afuna. (lmd phunzilo 1 mfundo 4)
5. Kuyambitsa Makambilano
(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Khalani okonzeka kusintha makambilano munthu akakuuzani kuti sakhulupilila Mulungu. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)
6. Kupanga Ophunzila
(Mph. 5) lff phunzilo 15 mfundo 4 (lmd phunzilo 11 mfundo 3)
Nyimbo 127
7. Khalani Okhulupilika Mukatamandidwa
(Mph. 7) Kukambilana.
Tambitsani VIDIYO yakuti Khalani Okhulupilika Mukatamandidwa, Monga Anacitila Yesu. Kenako funsani omvela kuti:
Kodi mwaphunzila ciyani kwa Sergei poona mmene anacitila zinthu modzicepetsa atatamandidwa?
8. Kampeni Yapadela Yoyambitsa Maphunzilo a Baibo mu September Poseŵenzetsa Buku la Kondwelani na Moyo Kwamuyaya!
(Mph. 8) Nkhani yokambidwa na woyang’anila utumiki. Limbikitsani ofalitsa kutengako mbali pa kampeniyi ndipo fotokozani makonzedwe a pa mpingo wanu.
9. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 14 ¶7-10, bokosi pa tsa. 110