Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

August 26–September 1

MASALIMO 78

August 26–September 1

Nyimbo 97 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Citsanzo Coticenjeza ca Aisiraeli Osakhulupilika

(Mph. 10)

Aisiraeli anaiŵala nchito zodabwitsa za Yehova (Sal. 78:​11, 42; w96-CN 12/1 29-30)

Aisiraeli sanayamikile zimene Yehova anawapatsa (Sal. 78:19; w06-CN 7/15 17 ¶16)

Aisiraeli sanaphunzilepo kanthu pa zolakwa zawo. M’malo mwake, anali kukhala osakhulupilika nthawi zambili (Sal. 78:​40, 41, 56, 57; w11-CIN 7/1 10 ¶3-4)


ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: N’ciyani cingatithandize kupewa kukhala osakhulupilika kwa Yehova?

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 78:​24, 25—N’cifukwa ciyani mana amachedwa “tiligu wocokela kumwamba” ndiponso “cakudya ca amphamvu”? (w06-CN 7/15 11 ¶5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo ziti zothandiza zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 78:​1-22 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Yambitsani phunzilo la Baibo. (lmd phunzilo 5 mfundo 5)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Seŵenzetsani kathilakiti poyambitsa makambilano. Yambitsani phunzilo la Baibo. (lmd phunzilo 5 mfundo 4)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 1) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwini nyumba wakuuzani kuti mukambe mwacidule. Yambitsani phunzilo la Baibo. (lmd phunzilo 2 mfundo 5)

7. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Popanda kukamba coonadi ca m’Baibo, pezani njila imene ingathandize munthu amene mukukamba naye kudziŵa kuti ndinu wa Mboni za Yehova, kenako yambitsani phunzilo. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 96

8. Phunzilani pa Citsanzo ca Mlaliki Filipo

(Mph. 15) Kukambilana.

M’Malemba muli zitsanzo zambili zabwino na zoipa. Kuti titengepo phunzilo pa zitsanzo zimenezi, tiyenela kupatula nthawi komanso kucita khama. Kuwonjezela pa kuŵelenga nkhani za m’Baibo, tiziganizila zimene tiphunzilapo na kupanga masinthidwe ofunikila.

Mlaliki Filipo anali Mkhristu wodziŵika kuti anali na “mzimu komanso nzelu.” (Mac. 6:​3, 5) Kodi tiphunzilapo ciyani pa citsanzo cake?

Tambitsani VIDIYO yakuti Zimene Tingaphunzile kwa Iwo—Mlaliki Filipo. Ndiyeno funsani omvetsela zimene aphunzilapo pa mbali zotsatila izi:

  • Zimene Filipo anacita zinthu zitasintha mwadzidzidzi.—Mac. 8:​1, 4, 5

  • Madalitso amene Filipo anapeza cifukwa cokhala wokonzeka kupita kumene kunali kufunikila anchito ambili.—Mac. 8:​6-8, 26-31, 34-40

  • Mapindu amene Filipo na banja lake anapeza cifukwa cokhala woceleza.—Mac. 21:​8-10

  • Cimwemwe cimene banja la muvidiyo iyi linapeza kaamba kotsatila citsanzo ca Filipo

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 14 ¶11-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 101 na Pemphelo