Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

August 5-11

MASALIMO 70-72

August 5-11

Nyimbo 59 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. ‘Uzani M’badwo Wotsatila’ za Mphamvu za Mulungu

(Mph. 10)

Ali mnyamata, Davide anaona thandizo la Yehova (Sal. 71:5; w99-CN 9/1 18 ¶17)

Mu ukalamba wake, Davide anaona thandizo la Yehova (Sal. 71:9; g04-CN 10/8 23 ¶3)

Davide analimbikitsa acinyamata mwa kuwauzako zocitika za pa umoyo wake (Sal. 71:​17, 18; w14 1/15 23 ¶4-5)

DZIFUNSENI KUTI, ‘Mu mpingo mwathu, n’ndani amene wakhala akutumikila Yehova kwa zaka zambili amene ningakonde kumufunsa mafunso pa kulambila kwathu kwa pabanja?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 72:8—Kodi zimene Yehova analonjeza Abulahamu pa Genesis 15:18 zinakwanilitsika bwanji mu ulamulilo wa Mfumu Solomo? (it-1-E 768)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 71:​1-24 (th phunzilo 5)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Ngati munthu wayambitsa mkangano, thetsani makambilanowo mwamtendele. (lmd phunzilo 4 mfundo 5)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) ULALIKI WAMWAYI. Pitilizani kukambilana na wacibale amene akuwayawaya kuyamba kuphunzila Baibo. (lmd phunzilo 8 mfundo 4)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 5) Nkhani. ijwfq 49—Mutu: N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Anasintha Zinthu Zina Zomwe Anali Kukhulupilila? (th phunzilo 17)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 76

7. Zimene Mungacite pa Kulambila kwa Pabanja

(Mph. 15) Kukambilana.

Nthawi ya kulambila kwa pabanja ni nthawi yofunika kuti ana ‘apatsidwe malangizo komanso kuphunzitsidwa mogwilizana ndi zimene Yehova amanena.’ (Aef. 6:4) Kuphunzila kumafuna khama, koma kungakhale kosangalatsa, maka-maka pamene ana akulitsa cikhumbo cawo cofuna kudziŵa coonadi ca m’Baibo. (Yoh. 6:27; 1 Pet. 2:2) Fotokozani mfundo zili m’bokosi lakuti “ Zimene Mungacite pa Kulambila kwa Pabanja,” zimene zingathandize makolo kuti kulambila kwawo kwa pabanja kuzikhala kothandiza komanso kokondweletsa. Kenako kambilanani mafunso awa:

  • Pa zimene takambilanazi, kodi mungafune kuyesako ziti?

  • Kodi mwapeza cina cake cothandiza?

Tambitsani VIDIYO yakuti Pitilizani Kupangitsa Kulambila kwa Pabanja Kukhala Kopindulitsa. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mwamuna angacite ciyani kuti mkazi wake azikondwela na kulambila kwa pabanja ngakhale kuti pa nyumba palibe ana?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 13 ¶17-24

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 123 na Pemphelo