July 1-7
MASALIMO 57-59
Nyimbo 148 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Yehova Amasokoneza Olimbana na Anthu Ake
(Mph. 10)
Davide anakakamizika kuthaŵa Mfumu Sauli (1 Sam. 24:3; Sal. 57, tumawu twapamwamba)
Yehova analepheletsa ziwembu za anthu amene anali kulimbana na Davide (1 Sam. 24:7-10, 17-22; Sal. 57:3)
Nthawi zambili ziwembu za anthu olimbana nafe sizikwanilitsa colinga cawo (Sal. 57:6; bt-CN 220-221 ¶14-15)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Ningaonetse bwanji kuti nimadalila Yehova pamene nikuzunzidwa?’—Sal. 57:2.
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
Sal. 57:7—Kodi kukhala wotsimikiza mtima kumatanthauza ciyani? (w23.07 18-19 ¶16-17)
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 59:1-17 (th phunzilo 12)
4. Khama—Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli
(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO, kenako kambilanani lmd phunzilo 7 mfundo 1-2.
5. Khama—Tengelani Citsanzo ca Paulo
(Mph. 8) Makambilano ozikika mu lmd phunzilo 7 mfundo 3-5, komanso mbali yakuti “Onaninso Malemba Awa.”
Nyimbo 65
6. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 15)
7. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 12 ¶1-6, bokosi pa tsa. 96