Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

July 15-21

MASALIMO 63-65

July 15-21

Nyimbo 108 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. “Cikondi Canu Cokhulupilika Nʼcabwino Kuposa Moyo”

(Mph. 10)

Kukhala pa ubale wabwino na Mulungu n’kofunika kwambili kuposa moyo (Sal. 63:3; w01-CN 10/15 15-16 ¶17-18)

Kuganizila kwambili mmene Yehova wationetsela cikondi cake cokhulupilika kapena kuti cosasintha kudzatithandiza kumuyamikila kwambili (Sal. 63:6; w19.12 28 ¶4; w15 10/15 22 ¶7)

Kuyamikila cikondi cosasintha ca Mulungu kumatilimbikitsa kumutamanda mokondwela (Sal. 63:​4, 5; w09-CN 7/15 16 ¶6)

ZIMENE MUNGACITE PA KULAMBILA KWA PABANJA: Kambilanani mmene Yehova wakuonetselani cikondi cosasintha.

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 64:3—Kodi vesiyi itilimbikitsa bwanji kuti tizilankhula mawu olimbikitsa nthawi zonse? (w07-CN 11/15 15 ¶6)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 63:1–64:10 (th phunzilo 12)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwini nyumba salankhula cinenelo canu. (lmd phunzilo 3 mfundo 4)

5. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 2) ULALIKI WAMWAYI. Makambilano atha musanamulalikile n’komwe. (lmd phunzilo 2 mfundo 4)

6. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAPOYELA. Dziŵani nkhani imene ingamucititse cidwi munthuyo, ndipo panganani kuti mukakambilanenso naye pa nthawi ina. (lmd phunzilo 1 mfundo 5)

7. Kufotokoza Zimene Mumakhulupilila

(Mph. 4) Citsanzo. ijwfq 51—Mutu: N’cifukwa Ciyani a Mboni za Yehova Amalalikila Anthu Omwe Anaŵauzapo Kale Kuti Safuna Kuŵalalikila? (lmd phunzilo 4 mfundo 3)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo Yakuti “Cikondi Sicitha” (ya pamisonkhano)

8. Mmene Timaonetsela Kuti Timakonda Mulungu

(Mph. 15) Kukambilana.

Yehova ni “wacikondi cokhulupilika coculuka.” (Sal. 86:15) Mawu akuti “cikondi cokhulupilika” kapena kuti cikondi cosasintha, amatanthauza cikondi cimene cimaonetsedwa cifukwa ca kudzipeleka, kukhulupilika, kusasunthika, komanso kugwilizana kwambili. Ngakhale kuti Yehova amakonda anthu onse, iye amaonetsa cikondi cimeneci kwa atumiki ake okha, anthu amene ali naye pa ubale wolimba. (Sal. 33:18; 63:3; Yoh. 3:16; Mac. 14:17) Tingasonyeze kuti timayamikila cikondi cosasintha ca Yehova mwa kuonetsa kuti nafenso timamukonda. Motani? Mwa kumvela malamulo ake, kuphatikizapo lamulo la ‘kupanga ophunzila.’—Mat. 28:19; 1 Yoh. 5:3.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Ulaliki. Kenako funsani omvela kuti:

Kodi cikondi cingatilimbikitse bwanji kulalikila uthenga wabwino

  • tikakhala olema?

  • tikamatsutsidwa?

  • tikamagwila nchito za tsiku na tsiku?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

(Mph. 30) bt mutu 12 ¶14-20

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 79 na Pemphelo