Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

July 22-28

MASALIMO 66-68

July 22-28

Nyimbo 7 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yehova Amanyamula Katundu Wathu Tsiku na Tsiku

(Mph. 10)

Yehova amamvela mapemphelo athu na kuwayankha (Sal. 66:19; w23.05 12 ¶15)

Yehova amadziŵa zosoŵa za anthu ovutika (Sal. 68:5; w10-CN 12/1 23 ¶6; w09-CN 4/1 31 ¶1)

Iye amatithandiza tsiku lililonse (Sal. 68:19; w23.01 19 ¶17)

ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: Kodi timamulola bwanji Yehova kunyamula katundu wathu?

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 68:18—Mu Isiraeli wakale, kodi ndani anali “mphatso za amuna”? (w06-CN 6/1 10 ¶5)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 66:​1-20 (th phunzilo 11)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) KUNYUMBA NA NYUMBA. Mwini nyumba ni wacikhalidwe cosiyana na canu. (lmd phunzilo 5 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Pitilizani kukambilana kathilakiti kamene munamusiyila ulendo wapita. (lmd phunzilo 9 mfundo 3)

6. Kupanga Ophunzila

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 102

7. Kodi Mungam’peputsileko Katundu Mkhristu Mnzanu?

(Mph. 15) Kukambilana.

Palibe mtumiki wa Mulungu yemwe amakhala yekha akamalimbana na mavuto. (2 Mbiri 20:15; Sal. 127:1) Yehova ni Mthandizi wathu. (Yes. 41:10) Kodi Yehova amatithandiza m’njila ziti? Amatipatsa malangizo poseŵenzetsa mawu ake na gulu lake. (Yes. 48:17) Amatipatsanso mzimu wake woyela wamphamvu. (Luka 11:13) Amagwilitsa nchito abale na alongo athu kuti atilimbikitse na kutithandiza. (2 Akor. 7:6) Izi zionetsa kuti Yehova angagwilitse nchito aliyense wa ife kupeputsako katundu wa Mkhristu mnzake.

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Okalamba. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti mum’peputsileko katundu Mkhristu wokalamba?

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Atumiki Anthawi Zonse. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti mum’peputsileko katundu mtumiki wanthawi zonse?

Tambitsani VIDIYO yakuti Onetsani Cikondi Cosatha mu Mpingo—Kwa Alendo Ocokela ku Maiko Ena. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi mungacite ciyani kuti muŵapeputsileko katundu anthu amene akukumana na mayeso ovuta?

8. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 88 na Pemphelo