July 29–August 4
SALIMO 69
Nyimbo 13 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)
1. Salimo 69 Inakambilatu Zocitika pa Umoyo wa Yesu
(Mph. 10)
Anthu anadana naye Yesu popanda cifukwa (Sal. 69:4; Yoh. 15:24, 25; w11-CN 8/15 11 ¶17)
Yesu anali wodzipeleka pa nyumba ya Yehova (Sal. 69:9; Yoh. 2:13-17; w10-CN 12/15 8 ¶7-8)
Yesu anavutika kwambili mu mtima ndipo anamupatsa vinyo wosakaniza na ndulu (Sal. 69:20, 21; Mat. 27:34; Luka 22:44; Yoh 19:34; g95-E 10/22 31 ¶4; it-2-E 650)
ZOFUNIKA KUZISINKHASINKHA: N’cifukwa ciyani Yehova anaikamo maulosi okamba za Mesiya m’Malemba a Ciheberi?
2. Kufufuza Cuma Cauzimu
(Mph. 10)
-
Sal. 69:30, 31—Kodi mavesi aya angatithandize bwanji kukonza mapemphelo athu kuti azikhala abwino? (w99-CN 1/15 18 ¶11)
-
Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?
3. Kuŵelenga Baibo
(Mph. 4) Sal. 69:1-25 (th phunzilo 2)
4. Kuleza Mtima—Mmene Yesu Anaonetsela Khalidwe Limeneli
(Mph. 7) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO, kenako kambilanani lmd phunzilo 8 mfundo 1-2.
5. Kuleza Mtima—Tengelani Citsanzo ca Yesu
(Mph. 8) Makambilano ozikika mu lmd phunzilo 8 mfundo 3-5, komanso mbali yakuti “Onaniso Malemba Awa.”
Nyimbo 134
6. Zofunikila za Mpingo
(Mph. 5)
7. Mfundo Zothandiza Pocita Kulambila kwa Pabanja
(Mph. 10) Kukambilana.
Mu January 2009, Phunzilo la Baibo la Mpingo linaphatikizidwa na Sukulu ya Utumiki wa Mulungu komanso Msonkhano wa Utumiki, kuti ukhale msonkhano umodzi wa mkati mwa mlungu. Izi zinathandiza mabanja kukhala na tsiku limodzi pa mlungu loti azicita kulambila kwa pabanja. Ambili ayamikila makonzedwe amenewa, amene anapangidwa kuti awathandize kuyandikila Yehova komanso kulimbitsa mgwilizano m’banja.—Deut. 6:6, 7.
Ni mfundo ziti zimene zingathandize mitu ya mabanja kucititsa kuti kulambila kwa pabanja kukhale kolimbikitsa?
-
Muzicita nthawi zonse. Ngati n’kotheka, khazikitsani tsiku limodzi lomwe muzicita kulambila kwa pabanja mlungu uliwonse. Ngati pa zifukwa zina mwalephela kucita kulambila kwa pabanja pa tsiku limene munasankha, sankhani tsiku lina
-
Muzikonzekela. Muzifunsako akazi anu zimene angakonde kucita pa kulambila kwa pabanja, ndipo nthawi zina muzifunsako ana anu. Simufunika kucita kukonzekela zambili, maka-maka ngati a m’banja lanu amakondwela kucita zinthu zolinganako mlungu uliwonse
-
Muzikonza pulogilamu mogwilizana na zofunika za m’banja lanu. Ana akamakula, zimene amafunikila komanso zimene angakwanitse kucita zimasintha. Pulogilamu yanu iyenela kuthandiza aliyense m’banja kukula kuuzimu
-
Muzikhala acikondi ndipo muzithandiza onse kukhala omasuka. Nthawi zina, ngati nyengo ilola mukhoza kucita kulambila kwa pabanja muli panja. Muzipumulako ngati m’pofunikila kutelo. Ngakhale kuti kukambilana mavuto amene mwaona m’banja n’kofunika, musaseŵenzetse nthawi ya kulambila kwa pabanja kukalipila ana anu kapena kuwapatsa uphungu
-
Muzicita zinthu zosiyana-siyana. Mwa citsanzo, mungakonzekele mbali ya msonkhano wotsatila, mungatambe na kukambilana vidiyo ya pa jw.org, kapena mungakozekele zimene mungakambe mu ulaliki. Nthawi zambili zocita pa kulambila kwa pabanja ziyenela kukhala zokambilana. Koma nthawi zina mungakonze zakuti aliyense acite phunzilo la munthu mwini
Kambilanani funso ili:
-
Kodi mwacita zotani kuti mugwilitse nchito mfundo izi pa pulogilamu yanu ya kulambila kwa pabanja?
8. Phunzilo la Baibo la Mpingo
(Mph. 30) bt mutu 13 ¶8-16, bokosi pa tsa. 105