Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

July 8-14

MASALIMO 60-62

July 8-14

Nyimbo 2 na Pemphelo | Mawu Oyamba (Mph. 1)

CUMA COPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

1. Yehova Amatiteteza, Amaticinjiliza, Ndiponso Amatilimbitsa

(Mph. 10)

Yehova ali ngati nsanja yolimba (Sal. 61:3; it-2-E 1118 ¶7)

Yehova amatilola kukhala alendo mu tenti yake (Sal. 61:4; it-2-E 1084 ¶8)

Yehova ali monga thanthwe (Sal. 62:2; w02-CN 4/15 16 ¶14)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi umoyo wanga wasintha bwanji n’kukhala wabwino cifukwa codziŵa Yehova na kumudalila?’

2. Kufufuza Cuma Cauzimu

(Mph. 10)

  • Sal. 62:11—Kodi “mphamvu ndi za Mulungu” m’lingalilo lotani? (w06-CN 6/1 11 ¶8)

  • Pa kuŵelenga Baibo kwa mlungu uno, munapeza mfundo zothandiza ziti zimene mungakonde kutifotokozelako?

3. Kuŵelenga Baibo

(Mph. 4) Sal. 60:1–61:8 (th phunzilo 10)

CITANI KHAMA PA ULALIKI

4. Kuyambitsa Makambilano

(Mph. 3) ULALIKI WAMWAYI. Yambitsani makambilano pambuyo pakuti munthu wakuonetsani kukoma mtima. (lmd phunzilo 2 mfundo 3)

5. Kubwelelako

(Mph. 4) KUNYUMBA NA NYUMBA. Uzani mwini nyumba za JW Library®, ndipo muonetseni mmene angaicitile daunilodi. (lmd phunzilo 7 mfundo 4)

6. Nkhani

(Mph. 5) w22.02 4-5 ¶7-10—Mutu: Khulupililani Yehova Mukalandila Malangizo. (th phunzilo 20)

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Nyimbo 12

7. Palibe ‘Cingatilekanitse ndi cikondi ca Mulungu’

(Mph. 10) Kukambilana.

Tambitsani VIDIYO. Kenako funsani omvela kuti:

  • Kodi Yehova anamuthandiza bwanji M’bale Nyirenda pamene anali kuzunzidwa?

8. Khala Bwenzi la Yehova—Zoyenela Kucita Kuti Ubatizike

(Mph. 5) Kukambilana. Tambitsani VIDIYO. Ndiyeno, ngati n’kotheka, pemphani ana amene munaŵasankhilatu kuti abwele ku pulatifomu ndipo afunseni kuti: Ngati ufuna kubatizika, kodi cofunika kwambili n’ciyani kuposa msinkhu wako? Ni zinthu zina ziti zomwe uyenela kucita kuti ubatizike?

9. Phunzilo la Baibo la Mpingo

Mawu Othela (Mph. 3) | Nyimbo 63 na Pemphelo