UMOYO NA UTUMIKI WATHU–KABUKU KA MISONKHANO June 2016
Maulaliki a Citsanzo
Maulaliki acitsanzo ogaŵila Galamukani! ndi tumapepala twauthenga. Seŵenzetsani maulaliki acitsanzo pokonza ulaliki wanu.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Khulupililani Yehova Ndipo Citani Zabwino
Seŵenzetsani malangizo a pa Salimo 37.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Kunola Luso Lathu mu Ulaliki—Kuseŵenzetsa Mavidiyo Pophunzitsa
N’cifukwa ciani tifunika kuseŵenzetsa mavidiyo mu ulaliki? Kodi angatithandize bwanji kunola luso lathu lophunzitsa?
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Yehova Amathandiza Odwala
Mau ouzilidwa amene Davide analemba pa Salimo 41, angalimbikitse atumiki okhulupilika a Mulungu amene ni odwala kapena amene akumana ndi mavuto.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
Yehova Sadzanyoza Munthu Wosweka Mtima
Pa Salimo 51, Davide anafotokoza mmene chimo linam’khudzila. N’ciani cinam’thandiza kuti acile kuuzimu?
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
Ufumu wa Mulungu Wakwanitsa Zaka Zoposa 100
Gwilitsilani nchito mafunso pokambilana zimene Ufumu wa Mulungu wacita kuyambila mu 1914.
CUMA COPEZEKA M’MAU A MULUNGU
“Umutulile Yehova Nkhawa Zako”
Malangizo ouzilidwa a Davide a pa Salimo 55:22 angatithandize kulimbana ndi mavuto kapena nkhawa.
UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Mulungu Ndiye Mthandizi Wanga”
Davide anatamanda Yehova cifukwa ca mau Ake. Ni mavesi ati a m’Baibulo amene anakuthandizani pamene munakumana ndi mavuto?